NOVODOR FC wolimbana ndi nankafumbwe wa mbatata
Sindikuganiza kuti ndikuyenera kulongosola za nankafumbwe owononga mbewu ya mbatata (Leptinotarsa decemlineata) popeza aliyense akudziwa za chirombo choipachi chimene chimaononga kwambiri mbatata ndipo sikotheka kuzigonjetsa popanda kugwiritsa ntchito mankhwala. Panopa, palibe akudziwa mankhwala enieni amene angagwiritsidwe ntchito pophera nankafumbwe owononga mbewuyu.
Lolemba 12. November 2012 12:21 | purintani | Tizilombo towononga mbewu
Kudzala mababu a maluwa ndi mmera
Chotsani mababu a maluwa ndi mmera amene mwalandira pa positi muphukusi, ndipo zisiyeni zikhale mumthunzi kwa masiku awiri kapena atatu. Chothekera chachiwiri ndikuzidzala nthawi yomweyo ndikuzisunga mumthunzi kwa masiku ochepa kuti zisafote ndi dzuwa.
Loweruka 26. November 2011 14:03 | purintani | Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Kulima bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus)
Bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus) ndi wotchuka kuposa bowa wamba (champignon mushroom)! tsopano. Kutengera ndi bowa wamba, bowa wa mzikuni uli ndi ubwino umodzi waukulu – sungasokonezedwe ndi chinthu chokupha (Amanita phalloides).
Pongamia pinnata
Pongamia pinnata
Chinsense Pongamia pinnata (maina ena: Honge Tree, Pongam Tree, Panigrahi) ndi mtengo umene umapululuka masamba nyengo yozizira, pakati pa mamitala 15–25 kutalika, umene uli m’gulu la Fabaceae. Uli ndi m’mwamba mwamukulu ndi maluwa ang’onoang’ono ambiri oyera, pinki kapena violet. Unabadwa ku India, koma unafalikira kulimidwa ku m’mwera chakuvuma kwa Asia.
Lachinayi 24. November 2011 19:59 | purintani | Zomera za chilendo
Kalimidwe ka Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia)
The Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia) ndizomera mmadzi zimene masamba ake amaoneka ngati clover. Mukuganiza kuti pakati pa zomera zammadzi ndi clover palibe ubale? Mbali ina – zonse mwa zinthuzi zikukamba za chikhalidwe cha zomera zosapezekapezeka zokongola kwambiri mu ulimi.
Lachitatu 23. November 2011 19:58 | purintani | Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Kudzala nthanga za mango
Mudzale nthanga za mango zongochotsedwa kumene kuti zimere bwino. Viyikani nthanga m’madzi ndi temperature yokwana 20–25°C kwa pafupifupi maola awiri mpaka asanu ndi imodzi.
Lachiwiri 22. November 2011 19:57 | purintani | Zomera za chilendo, Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Mango a Kalimantan, Kasturi (Mangifera casturi)
Mango a Kalimantan (Mangifera casturi) kapena mu chilankhulo cha kuderako otchedwa Kasturi ndi mtengo wa zipatso opezeka kumadera otentha wautali 10–30 m umapezeka kawirikawiri kudera laling’ono lozungulira Banjarmasin ku Southern Borneo (Indonesia). Masiku ano supezekanso mchire chifukwa chakusavomerezekwa kodula zipika. Ngakhale zili chomwechi, ukulimidwabe m’derali chifukwa cha zipatso zake zokoma.
Lolemba 21. November 2011 19:55 | purintani | Zomera za chilendo
Mango aku Indonesia
Pachilumba cha Borneo ku Indonesia pali mitundu ya mango yokwana makumi atatu ndi mphambu zinayi (Mangifera) yomwe ndi yachilengedwe. Mitundu yambiri ili pachiwopsyezo cha kusapezekanso chifukwa cha kugwetsedwa kwa mitengo. Ina mwa mitundu ya mangowa, monga mango a Kalimantan (Mangifera casturi) atha kale mutchire, sakupezekamo.
Mitengo ina ya mango yochokera ku Borneo ndi monga Mangifera griffithi (yodziwika ndi maina awa: asem raba, ndi romian), Mangifera pajang (asem payang), Mangifera quadrifida (asem kipang) ndi Mangifera torquenda (asem putaran).
Fodya wa Mtengo Nicotiana glauca – Chomera chokongoletsa pamalo perspective!
Fodya wa Mtengo (Nicotiana glauca)
Khumbo la munthu ku chinthu chatsopano ndi chosachitikachitika lilibe malire. Alimi naonso amalota za chinthu chatsopano chimene angalime mmunda mwawo – chimene aliyense alibe. Msika wa mbewu nawonso umakhala ndi zinthu zatsopano za alimi – ndi cholinga choletsa njala imene alimi ofuna zinthu zabwino amakhala nayo. Kukhanzikitsidwa kwa malonda a mbewu zatsopano, kudzapangitsa kuti mitengo ya fodya izipezeka paliponse kwa alimi onse posachedwapa!
Loweruka 19. November 2011 19:31 | purintani | Zomera za chilendo
Ulimi wa Welwitschia mirabilis
Mbewu ya Welwitschia
Welwitschia (Welwitschia mirabilis) ndichomera chomwe chimamera ndi kukula m’kadera kakang’ono ka m‘mbali mwa nyanja ya mchere ya Atlantic mdziko la Namibia ndi kummwera kwa Angola. Welwitschia ndi mtengo weni-weni, ngakhale kuti sumaoneka choncho ukauona koyamba. Chomerachi chimakhala ndi chithime chimodzi chachifupi pomwe pamamela masamba awiri – omwe amaoneka ngati ma riboni awiri opiringizika. Welwitschia nthawi zina amaoneka ngati mulu wa zinyalala!
Lachisanu 18. November 2011 19:14 | purintani | Zomera za chilendo
Mbiri ya KPR
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.
Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi