Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Chipatso cha mkate Artocarpus odoratissimus, Marang

Genus Chipatso cha mkate (Artocarpus) ali ndi mitundu kuzungulira 60 a mitengo yobiliwira kuchokera ku gulu la Moraceae (gulu la mulberry kapena gulu la nkhuyu). Amapezeka ku South East Asia ndi kuzilumba za Pacific Ocean. Ma Chipatso cha mkate ndi abale enieni a mitengo ya nkhuyuFicus. Chipatso cha mkate amene amalimidwa kwambiri ndi Artocarpus altilis. Mitundu ina yambiri monga Artocarpus communis, Artocarpus integer (Cempedak), Artocarpus heterophyllus (Jackfruit, Nangka) ndi Artocarpus odoratissimus (Marang) ilinso m’gulu la Chipatso cha mkate.

Lachinayi 17. November 2011 19:07 | purintani | Zomera za chilendo

Kodi mungatani ndi udzu / kapinga wotchetchedwa?

Ngati mumakonda kapinga wokongola, wamfupi ndi woyala bwino, muzitchetcha bwalo lanu mowilikiza. Panopa, udzu otchetchedwa pafupipafupi umabweretsa udzu wambiri umene umangokupatsa mavuto. Ndimangogwedeza mutu kusakhulupilira kuti anthu mosalabadira kuchotsa manyowa itchipitsitsa, otsika mtengo kwambiri.

Lachitatu 16. November 2011 19:25 | purintani | Udzu

Kodi mungatchetche bwanji bwalo lanu moyenera?

Kuli koyenera kutchetcha bwalo lanu moyenela kuti likhale ndi kapinga oyalana ndi odzadza bwino. Palibe mtengo wa conifer umene ungaoneke bwino utazunguliridwa ndi bwalo louma!

Musanatchetche bwalo, kumbukirani – udzu udulidwe mpaka kufika 1/3. Izi zikutanthauza kuti udzu kutali 6cm, ukuyenera kutchetchedwa kufika 4 cm. msinkhu wabwino wa udzu ndi 2–3 cm. ngati mukutchetcha pansi kwambiri, kapinga akhonza kuuma. Mukatha kutchetcha kapinga, muthilireni kwambiri (osachepera malita a madzi 10–15 pa sikweya mitala imodzi).

Lachiwiri 15. November 2011 19:23 | purintani | Udzu

Kudzala kapinga watsopano

Nthawi yabwino yodzala kapinga kapena udzu owonjezera pa kapinga yemwe alipo kale ku Ulaya ndi kuchokera mwezi wa Meyi mpaka Juni. Julaye akhonza kukhala nthawi yabwino kudzala ngati kuli mvula.

Lolemba 14. November 2011 19:21 | purintani | Udzu

Kodi ndikugwetsa bwanji nankafumbwe wa nyemba?

Sindikuyembekezera kuti simukuyenera kuuzidwa za nankafumbwe wa nyemba. Uyu ndi nankafumbwe wamkulu 3–4mm, amene amapezeka pa njere mukhitchini mwachitsanzo.

Anankafumbwe owonongawa amapangidwa kuchokera mmitundu ya makoko a njere kapena nthanga za zomera zosiyanasiyana. Tingoti, makoko aliwonse ali ndi zina mwa zirombozi – chitedze – nankafumbwe wa chitedze, sawawa – nankafumbwe wa sawawa, mseula – nankafumbwe wa mseula, ndi ena ambiri…

Lachinayi 3. November 2011 22:13 | purintani | Tizilombo towononga mbewu

Kiwano – Cucumis metuliferus

Zipatso za Kiwano zazitali 10–15 cm zimaoneka ngati malalanje. Zili mugulu la minkhaka. Zipatso zake zili ndi tinyanga tating’onoting’ono pa makoko ake ndipo zimamupangitsa munthu kuganizira za chida cha nkhondo. Mnofu wa chipatso ndiwobiliwira ndipo nthawi zambiri umakhala ndi njere zoyera zambiri zazitali 5–10mm.

Lachitatu 2. November 2011 20:56 | purintani | Zomera za chilendo

Mpoza (Annona cherimola)

Tsopano mitundu yosangalatsa ya zipatso za kumadera otentha ikutumizidwa ku Ulaya. Ndakwanitsa kugula chipatso cha mpoza ndikuchilawa. Sichipezeka m’mashopu a zipatso koma ndithokoze makondedwe anga, nachonso chipeza malo ake kumeneko!

Mipoza ndi maina otchulidwa kwambiri pa zipatso za Annona cherimola zomera m’zigwa za Andes kuchokera ku Colombia mpaka ku Peru pamtunda wa 700–2400 m. Umapiliranso matemperature wotsika kotero ukhonza kudzalidwa malo ambiri m’madera ena othentherapo padziko lonse – ngakhalenso ku Israel ndi kum‘mwera kwa Spain. Pamitundu imeneyi tikudziwa pafupifupi mitundu 120.

Lachiwiri 1. November 2011 20:51 | purintani | Zomera za chilendo

Tiyi waku China – Limani tiyi wanuwanu!

chithunzi

Maluwa a tiyi

Nyengo yozizira isanafike kumapeto, mlimi aliyense amaganizira za chomwe adzalime munyengo ikudzayo. Kodi mumaona kuti kulima tomato, paprika ndi minkhaka ndikosavuta? Kodi mukufuna china? China chachilendo? Mukuganiza bwanji pa zolima tiyi wanuwanu chaka chino?!

Lolemba 31. October 2011 20:48 | purintani | Zomera za chilendo

Mitengo ya palmu Rhapidophyllum hystrix yoyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri (Ma Needle Palm)

chithunzi

Rhapidophyllum hystrix

Rhapidophyllum hystrix ndi umodzi mwa mitundu ya palmu yoyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri. Pali mtundu umodzi okha mu gulu la Rhapidophyllum. Chilengedwe cha palmu ameneyu ndi malo ozizira a kum’mwera chakum’mawa kwa USA. Komabe, zikomo chifukwa cha kuyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri yomwe ili yotsika ngati –20 °C ndi mbewu yodziwika kwambiri pa dziko lonse lapansi, makamaka ku Europe.

Lachiwiri 19. May 2009 18:23 | purintani | Mapalmu

Pinus kesiya - Khasi Pine, Paini wa Khasi

Khasi Pine, Paini wa Khasi (Pinus kesiya) ndi mtundu wa mitengo okula mwachangu ochokera ku Asia, umene sumapezeka ukulimidwa kawirikawiri kunja kwa dziko lake. Mitengo yake imakhala pakatikati pa mamita 30–35 kutalika kwake ndipo thunthu lamtengo chikhonza kukwana mitala imodzi mu dayamita (diameter). Nthambi iliyonse ili ndi tinthambi ting’onoting’ono titatu – iliyonse yotalika masentimitala 15 mpaka 20. Zipatso za mitengo imeneyi (zibalobalo za mtengo wa paini) zimakhala zazitali ma sentimitala 5 mpaka 9 ndipo njere zake zimakhala zazitali masentimitala 1.5 mpaka 2.5.

Lachiwiri 19. May 2009 18:22 | purintani | Zomera za chilendo

Continue: 1-10 11-20 21-22

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi