Archive of all articles
There you can find all articles which are available in this language section of Botanix.
Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi
2012
November (1)2009
May (4)M’ndandanda wa mitu ya nkhani ya pa mwezi: November 2011 (16 textů)
Kudzala mababu a maluwa ndi mmera
Chotsani mababu a maluwa ndi mmera amene mwalandira pa positi muphukusi, ndipo zisiyeni zikhale mumthunzi kwa masiku awiri kapena atatu. Chothekera chachiwiri ndikuzidzala nthawi yomweyo ndikuzisunga mumthunzi kwa masiku ochepa kuti zisafote ndi dzuwa.
Loweruka 26. November 2011 14:03 | purintani | Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Kulima bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus)
Bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus) ndi wotchuka kuposa bowa wamba (champignon mushroom)! tsopano. Kutengera ndi bowa wamba, bowa wa mzikuni uli ndi ubwino umodzi waukulu – sungasokonezedwe ndi chinthu chokupha (Amanita phalloides).
Pongamia pinnata
Pongamia pinnata
Chinsense Pongamia pinnata (maina ena: Honge Tree, Pongam Tree, Panigrahi) ndi mtengo umene umapululuka masamba nyengo yozizira, pakati pa mamitala 15–25 kutalika, umene uli m’gulu la Fabaceae. Uli ndi m’mwamba mwamukulu ndi maluwa ang’onoang’ono ambiri oyera, pinki kapena violet. Unabadwa ku India, koma unafalikira kulimidwa ku m’mwera chakuvuma kwa Asia.
Lachinayi 24. November 2011 19:59 | purintani | Zomera za chilendo
Kalimidwe ka Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia)
The Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia) ndizomera mmadzi zimene masamba ake amaoneka ngati clover. Mukuganiza kuti pakati pa zomera zammadzi ndi clover palibe ubale? Mbali ina – zonse mwa zinthuzi zikukamba za chikhalidwe cha zomera zosapezekapezeka zokongola kwambiri mu ulimi.
Lachitatu 23. November 2011 19:58 | purintani | Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Kudzala nthanga za mango
Mudzale nthanga za mango zongochotsedwa kumene kuti zimere bwino. Viyikani nthanga m’madzi ndi temperature yokwana 20–25°C kwa pafupifupi maola awiri mpaka asanu ndi imodzi.
Lachiwiri 22. November 2011 19:57 | purintani | Zomera za chilendo, Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Mango a Kalimantan, Kasturi (Mangifera casturi)
Mango a Kalimantan (Mangifera casturi) kapena mu chilankhulo cha kuderako otchedwa Kasturi ndi mtengo wa zipatso opezeka kumadera otentha wautali 10–30 m umapezeka kawirikawiri kudera laling’ono lozungulira Banjarmasin ku Southern Borneo (Indonesia). Masiku ano supezekanso mchire chifukwa chakusavomerezekwa kodula zipika. Ngakhale zili chomwechi, ukulimidwabe m’derali chifukwa cha zipatso zake zokoma.
Lolemba 21. November 2011 19:55 | purintani | Zomera za chilendo
Mango aku Indonesia
Pachilumba cha Borneo ku Indonesia pali mitundu ya mango yokwana makumi atatu ndi mphambu zinayi (Mangifera) yomwe ndi yachilengedwe. Mitundu yambiri ili pachiwopsyezo cha kusapezekanso chifukwa cha kugwetsedwa kwa mitengo. Ina mwa mitundu ya mangowa, monga mango a Kalimantan (Mangifera casturi) atha kale mutchire, sakupezekamo.
Mitengo ina ya mango yochokera ku Borneo ndi monga Mangifera griffithi (yodziwika ndi maina awa: asem raba, ndi romian), Mangifera pajang (asem payang), Mangifera quadrifida (asem kipang) ndi Mangifera torquenda (asem putaran).
Fodya wa Mtengo Nicotiana glauca – Chomera chokongoletsa pamalo perspective!
Fodya wa Mtengo (Nicotiana glauca)
Khumbo la munthu ku chinthu chatsopano ndi chosachitikachitika lilibe malire. Alimi naonso amalota za chinthu chatsopano chimene angalime mmunda mwawo – chimene aliyense alibe. Msika wa mbewu nawonso umakhala ndi zinthu zatsopano za alimi – ndi cholinga choletsa njala imene alimi ofuna zinthu zabwino amakhala nayo. Kukhanzikitsidwa kwa malonda a mbewu zatsopano, kudzapangitsa kuti mitengo ya fodya izipezeka paliponse kwa alimi onse posachedwapa!
Loweruka 19. November 2011 19:31 | purintani | Zomera za chilendo
Ulimi wa Welwitschia mirabilis
Mbewu ya Welwitschia
Welwitschia (Welwitschia mirabilis) ndichomera chomwe chimamera ndi kukula m’kadera kakang’ono ka m‘mbali mwa nyanja ya mchere ya Atlantic mdziko la Namibia ndi kummwera kwa Angola. Welwitschia ndi mtengo weni-weni, ngakhale kuti sumaoneka choncho ukauona koyamba. Chomerachi chimakhala ndi chithime chimodzi chachifupi pomwe pamamela masamba awiri – omwe amaoneka ngati ma riboni awiri opiringizika. Welwitschia nthawi zina amaoneka ngati mulu wa zinyalala!
Lachisanu 18. November 2011 19:14 | purintani | Zomera za chilendo
Chipatso cha mkate Artocarpus odoratissimus, Marang
Genus Chipatso cha mkate (Artocarpus) ali ndi mitundu kuzungulira 60 a mitengo yobiliwira kuchokera ku gulu la Moraceae (gulu la mulberry kapena gulu la nkhuyu). Amapezeka ku South East Asia ndi kuzilumba za Pacific Ocean. Ma Chipatso cha mkate ndi abale enieni a mitengo ya nkhuyuFicus. Chipatso cha mkate amene amalimidwa kwambiri ndi Artocarpus altilis. Mitundu ina yambiri monga Artocarpus communis, Artocarpus integer (Cempedak), Artocarpus heterophyllus (Jackfruit, Nangka) ndi Artocarpus odoratissimus (Marang) ilinso m’gulu la Chipatso cha mkate.
Lachinayi 17. November 2011 19:07 | purintani | Zomera za chilendo
Kodi mungatani ndi udzu / kapinga wotchetchedwa?
Ngati mumakonda kapinga wokongola, wamfupi ndi woyala bwino, muzitchetcha bwalo lanu mowilikiza. Panopa, udzu otchetchedwa pafupipafupi umabweretsa udzu wambiri umene umangokupatsa mavuto. Ndimangogwedeza mutu kusakhulupilira kuti anthu mosalabadira kuchotsa manyowa itchipitsitsa, otsika mtengo kwambiri.
Kodi mungatchetche bwanji bwalo lanu moyenera?
Kuli koyenera kutchetcha bwalo lanu moyenela kuti likhale ndi kapinga oyalana ndi odzadza bwino. Palibe mtengo wa conifer umene ungaoneke bwino utazunguliridwa ndi bwalo louma!
Musanatchetche bwalo, kumbukirani – udzu udulidwe mpaka kufika 1/3. Izi zikutanthauza kuti udzu kutali 6cm, ukuyenera kutchetchedwa kufika 4 cm. msinkhu wabwino wa udzu ndi 2–3 cm. ngati mukutchetcha pansi kwambiri, kapinga akhonza kuuma. Mukatha kutchetcha kapinga, muthilireni kwambiri (osachepera malita a madzi 10–15 pa sikweya mitala imodzi).
Kudzala kapinga watsopano
Nthawi yabwino yodzala kapinga kapena udzu owonjezera pa kapinga yemwe alipo kale ku Ulaya ndi kuchokera mwezi wa Meyi mpaka Juni. Julaye akhonza kukhala nthawi yabwino kudzala ngati kuli mvula.
Kodi ndikugwetsa bwanji nankafumbwe wa nyemba?
Sindikuyembekezera kuti simukuyenera kuuzidwa za nankafumbwe wa nyemba. Uyu ndi nankafumbwe wamkulu 3–4mm, amene amapezeka pa njere mukhitchini mwachitsanzo.
Anankafumbwe owonongawa amapangidwa kuchokera mmitundu ya makoko a njere kapena nthanga za zomera zosiyanasiyana. Tingoti, makoko aliwonse ali ndi zina mwa zirombozi – chitedze – nankafumbwe wa chitedze, sawawa – nankafumbwe wa sawawa, mseula – nankafumbwe wa mseula, ndi ena ambiri…
Lachinayi 3. November 2011 22:13 | purintani | Tizilombo towononga mbewu
Kiwano – Cucumis metuliferus
Zipatso za Kiwano zazitali 10–15 cm zimaoneka ngati malalanje. Zili mugulu la minkhaka. Zipatso zake zili ndi tinyanga tating’onoting’ono pa makoko ake ndipo zimamupangitsa munthu kuganizira za chida cha nkhondo. Mnofu wa chipatso ndiwobiliwira ndipo nthawi zambiri umakhala ndi njere zoyera zambiri zazitali 5–10mm.
Lachitatu 2. November 2011 20:56 | purintani | Zomera za chilendo
Mpoza (Annona cherimola)
Tsopano mitundu yosangalatsa ya zipatso za kumadera otentha ikutumizidwa ku Ulaya. Ndakwanitsa kugula chipatso cha mpoza ndikuchilawa. Sichipezeka m’mashopu a zipatso koma ndithokoze makondedwe anga, nachonso chipeza malo ake kumeneko!
Mipoza ndi maina otchulidwa kwambiri pa zipatso za Annona cherimola zomera m’zigwa za Andes kuchokera ku Colombia mpaka ku Peru pamtunda wa 700–2400 m. Umapiliranso matemperature wotsika kotero ukhonza kudzalidwa malo ambiri m’madera ena othentherapo padziko lonse – ngakhalenso ku Israel ndi kum‘mwera kwa Spain. Pamitundu imeneyi tikudziwa pafupifupi mitundu 120.
Lachiwiri 1. November 2011 20:51 | purintani | Zomera za chilendo
Mbiri ya KPR
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.
Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi