Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Archive of all articles

There you can find all articles which are available in this language section of Botanix.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi

Author:

2009

May (4)

Gawo: Mapalmu

Nkhani za mitengo ya palmu

Mango aku Indonesia

Pachilumba cha Borneo ku Indonesia pali mitundu ya mango yokwana makumi atatu ndi mphambu zinayi (Mangifera) yomwe ndi yachilengedwe. Mitundu yambiri ili pachiwopsyezo cha kusapezekanso chifukwa cha kugwetsedwa kwa mitengo. Ina mwa mitundu ya mangowa, monga mango a Kalimantan (Mangifera casturi) atha kale mutchire, sakupezekamo.

Mitengo ina ya mango yochokera ku Borneo ndi monga Mangifera griffithi (yodziwika ndi maina awa: asem raba, ndi romian), Mangifera pajang (asem payang), Mangifera quadrifida (asem kipang) ndi Mangifera torquenda (asem putaran).

Lamulungu 20. November 2011 19:44 | purintani | Mapalmu

Mitengo ya palmu Rhapidophyllum hystrix yoyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri (Ma Needle Palm)

chithunzi

Rhapidophyllum hystrix

Rhapidophyllum hystrix ndi umodzi mwa mitundu ya palmu yoyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri. Pali mtundu umodzi okha mu gulu la Rhapidophyllum. Chilengedwe cha palmu ameneyu ndi malo ozizira a kum’mwera chakum’mawa kwa USA. Komabe, zikomo chifukwa cha kuyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri yomwe ili yotsika ngati –20 °C ndi mbewu yodziwika kwambiri pa dziko lonse lapansi, makamaka ku Europe.

Lachiwiri 19. May 2009 18:23 | purintani | Mapalmu

Palmu Parajubaea torallyi (Palma Chico, coconut wam’phiri la Bolivian)

Parajubaea torallyi ndi palmu wamphamvu wokongola ochokera ku m’mwera kwa America. Koma, siumalimidwa kawirikawiri ndi osamalira zomera a kunja kwa dziko la chilengedwe chake, Bolivia, chifukwa chakukula kwa masamba ake (kutanthauza kuti mtengo wake wotumizira ndiwokwera).

Lachiwiri 19. May 2009 18:16 | purintani | Mapalmu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi