Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Indian Lotus Nelumbo nucifera zomera za m’madzi

chithunzi

Duwa la Indian Lotus (zomera za m’madzi)

Ma Indian Lotus Nelumbo nucifera (zomera za m’madzi) ndi zomera zam’madzi zokongola zokhala ndi nthanga, masamba a girini omwe amayandama pamwamba pa madzi. Maluwa a pink amakonda kupezeka pa mtengo wokhuthala omwe wakwera ma centimeter ambiri pamwamba pa madzi.

Maluwa a Indian Lotus amagwiridwa mopembedzedwa ndipo amagwiritsidwa ntchito ndi anthu a mpingo waku India womwe unayambitsidwa ndi Buddha pa miyambo yawo. Chomera chose ndichokwanira kudya munthu; ngakhale makamaka nthanga ndi mizu zimakonda kugwiritsidwa pa miyambo yawo yamahikidwe ku mmwera chakumadzulo kwa Asia konse. Ma Indian Lotus ndizomera za m’matope zomwe zingamere ngati momwe amelera maluwa onunkhira a lile. Sizovuta kulima chomera chimenechi munyengo zathu; chongofunika ndikudziwa mapangidwe ake!

Kulima Indain Lotus kuchokera ku nthanga, chikopa cholimba chakunja kwa nthanga chikuyenera poyambilira kukhukhuzidwa pansi (kusisita kapena kukwecha) ndi pepala la mchenga. Izi zimathandiza kuti madzi azilowa mosavuta apo ayi nthanga sizingayambe kumera. Ngati chikhungu cholimba chakunjacho chili chosawonongeka, nthanga imakhala yamoyo nthawi yaitali, kwa zaka zaka. Komabe, ikayikidwa m’madzi, pakhonza kupita zaka zambiri kuti nthanga imasule.

chithunzi

kumasula nthanga za Indian Lotus

Mumadziwa bwanji kuti mwakwechetsa khungu mokwanira chikopa chakunja cha nthanga? Munthu akhonza kudziwa ndi saizi ya kukula kwa nthanga akangoyiyika m’madzi. Ngati nthanga yadabula kukula kwake m’maola 24, osakhulitsanso. Koma ngati siinakule mu saizi yake, mukuyenera kukhulabe, kenaka ndikuyika nthangayo m’madzi kwa maola 24 otsatira, kenaka onaninso saizi yake. Njira imeneyi ikuyenera kubwerenzedwa mpakana nthangala idabule saizi yake.

Nthanga zokha zimafuna madzi… Mukangokwanitsa kukwechetsa, viyikani nthanga muchitini cha madzi. M’pweya wa madzi poyambilira pakumasula kwa nthanga ndi pakati pa 27 °C ndi 28 °C (ngakhale nthanga ingadabulitse mu mpweya wa 20 °C basi). Pa mpweya imeneyi nthanga imabereka mwachangu ndipo pakutha pa mulungu umodzi, imamasula. Onani nkhani za zithunzi ku .

Masamba oyambilira akangoyamba kuwoneka, bzyalani nthanga yomwe yayamba kumera pamalo pomwe pali matope kapena dothi laku dambo, pansi pa chitini (dambo, chitsime). Madzi a muchitini akhale 30cm pamwamba pa dothi. Ngati mwagwiritsa ntchito dothi laku dambo, maluwa a Indian Lotus akhonza kumera mosavuta mu dziwe lodzadza ndi nsomba.

Pang’onopang’ono, chomera chija chikamakula, chidzafuna malo ambiri. Mukhonza kudzala muchitsime, mu dimba, mu nyumba ya mbewu, kapena malo ena ali onse osazizira. Kutentha kwake koyenelera kubzyala Indian Lotus ndi pakati pa 20°C ndi 35°C.

Indian Lotus akhonza kudzalidwa mudimba mu chaka chonse m’malo ambiri aku Africa. M’pweya ochepetsetsa usamachepere 0°C.

Malimidwe abwino a Indian Lotus ndi kugwiritsa ntchito miphika ya maluwa kugwira chili chonse kuchokera pa ma liters a madzi okwana 60 kapena 80. Gwiritsani ntchito njira iyi: Ikani nthanga yo/zoyamba kuphukirayo/zo pa matope kapena mu dothi laku dambo mkati mwa poto wa maluwa kenaka ikani poto wa maluwa mkati mwa choikamo zitini, cha simenti. Kuti zikule bwino, dzalitsani choikamo zitini za maluwacho ndi madzi mpaka pamwamba

Ubwino ogwiritsa ntchito choikamo zitini cha simenti ndiwakuti chikhonza kuikidwa malo ali onse. Chomera cha Indian Lotus chimatha kumera pena pali ponse – ngakhale m’nyumba!

Nkhani yotsatira: Palmu Parajubaea torallyi (Palma Chico, coconut wam’phiri la Bolivian) »»»

Lachiwiri 19. May 2009 17:58 | purintani | Zomera za m’madzi

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi