Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Kodi mungatchetche bwanji bwalo lanu moyenera?

Kuli koyenera kutchetcha bwalo lanu moyenela kuti likhale ndi kapinga oyalana ndi odzadza bwino. Palibe mtengo wa conifer umene ungaoneke bwino utazunguliridwa ndi bwalo louma!

Musanatchetche bwalo, kumbukirani – udzu udulidwe mpaka kufika 1/3. Izi zikutanthauza kuti udzu kutali 6cm, ukuyenera kutchetchedwa kufika 4 cm. msinkhu wabwino wa udzu ndi 2–3 cm. ngati mukutchetcha pansi kwambiri, kapinga akhonza kuuma. Mukatha kutchetcha kapinga, muthilireni kwambiri (osachepera malita a madzi 10–15 pa sikweya mitala imodzi).

Pano timagwiritsa ntchito mitundu iwiri ya zotchetchera – mtundu wachikalekale ndi wina wotchetcha mophimbira. Wotchetcha mophimbira ndi udzu wosatoledwa ukatchetchedwa, koma umadulidwa bwino lomwe ndikutayidwanso pabwalo lanu nthawi iliyonse imene mwatchetcha. Komabe, chotchetchera chimenechi sichoyenera ngati muli ndi dziwi losambapo (swimming pool), chifukwa udzuwo udzagwera mudwiwelo. Apa ndibwino kugwiritsa ntchito chotchetchera cha chikale chokhala ndi bokosi, limene limatola udzu umene watchetchedwa.

Palinso zotchetchera pabwalo zophatikizana zimene ungasankhe kugwiritsa ntchito bokoso lotolera kapena ayi.

Izi zimayenera mabwalo amene ali ndi mtsetse wa 15°. Ngati bwalo lanu liri malo otsetsereka, mugwiritse ntchito zotchetchera za manja zoyeneleranso malo ena ang’onoang’ono amene mungafikire ozungulira mitengo kapena mphepete mwa mabedi a maluwa.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Kudzala kapinga watsopano Nkhani yotsatira: Kodi mungatani ndi udzu / kapinga wotchetchedwa? »»»

Lachiwiri 15. November 2011 19:23 | purintani | Udzu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi