Mango a Kalimantan, Kasturi (Mangifera casturi)
Mango a Kalimantan (Mangifera casturi) kapena mu chilankhulo cha kuderako otchedwa Kasturi ndi mtengo wa zipatso opezeka kumadera otentha wautali 10–30 m umapezeka kawirikawiri kudera laling’ono lozungulira Banjarmasin ku Southern Borneo (Indonesia). Masiku ano supezekanso mchire chifukwa chakusavomerezekwa kodula zipika. Ngakhale zili chomwechi, ukulimidwabe m’derali chifukwa cha zipatso zake zokoma.
Mango a Kalimantan (Mangifera casturi) ndi ang’ono kuyerekeza ndi mitundu ina ya mango. Mango limodzi limalemera magaramu 50 mpaka 84. Akakhala kuti ndiawisi, mtundu wa chipatso umakhala wobiliwira – koma akaphya, mtundu umasintha kukhala wa burawuni kapena pepo wakuda ndipo ali ndi makoko owala, nthawi zambiri owoneka mwa pepo. Kapangidwe kake ka mtundu wa mangowa ndi chinthu chinanso mwa zinthu zina chimene chimasiyanitsa mango a M. casturi ndi mango ena. Pali mitundu itatu yomwe inalembedwa ya Mangifera casturi – Kasturi, Mangga Cuban ndi Pelipisan. Yotchuka kwambiri ndi Kasturi chifukwa cha fungo lake. Mangga Cuban ndi Pelipisan nthawi zambiri amaonedwa ngati osiyana mitundu. Pelipisan akhonza kukhala onunkhira ngati Kasturi zomwe zikuonetsa kuti chipatso chiyenera kukhala cha hybrid ya Kasturi. Kafukufuku wambiri akuyenera kuchitikabe kuti mango amenewa adziwike bwino-bwino.
Mnofu wa chipatsochi mtundu wake ndi orenji ndipo ndionunkhira bwino. Tikasiyanitsa Kasturi ndi Mango (Mangifera indica), Kasturi samatsekemera moposa koma amakometsetsa ndipo ali ndi fungo labwino. Mnofu wa Kasturi uli ndi mitsitsi yoposa.
Kasturi ndiwodziwika kwambiri pakati pa anthu aku South Borneo ndi Madera ozungulira. Kununkhira kwa zipatsozi ndikwabwino mokuti pali nyimbo yakale yokhudzana ndi zimenezi: “Seharum kasturi, seindah pelangi, semuanya bermula.” Kutanthauza kuti: “Oh, kununkhira ngati Kasturi, kukongola ngati mautawaleza. Chikondichi chayamba ulendo wake.”
Kugwetsa mitengo mwachisawawa kukupangitsa mitengo yamangowa kusowa mtchire. Mango akale a Kalimantan akhonza kutha mitengo yake ikamagwetsedwa chifukwa chakuchuluka kwa nkhuni zake. Mitengo imakonda kudzalidwa pang’ono ndi anthu wamba pakhomo pawo kapena m’minda ing’onoing’ono.
Kusiyana ndi mitengo ya zipatso yokula msanga, Mango a Kalimantan samalimidwa m’minda yaikulu ku Indonesia chifukwa amachedwa kukula. Minda ya Mango a Kalimantan imapezeka kudera lotchedwa Mataraman m’boma la Banjar basi (Boma la Banjar silofanana ndi boma la Banjarmasin). Anthu aku Mataraman anayesapo kulima pang’ono m’chaka cha 1980 ndipo kukolora koyamba kunali m’chaka cha 2005. Ngakhale zipatsochi zimapezeka zambiri, komabe sizimakwanira m’mene zimafunidwira.
Ntchito za mitengo ya Mango a Kalimantan ndizokwanira ku chipatso ndi nkhuni. Ngakhale mitengo yakale ikhonza kukhala ndi zitsa zoposa 1m, anthu aku Banjar (mbadwa za mkati ndi mphepete mwa Nyanja ku Southern Borneo), amakonda kugwiritsa ntchito zipatso zokha chifukwa mitengo imatenga nthawi yayitali kuti ikule. Pachifukwachi, anthu aku Banjar amapanga nkhuni mitengo ina yofanana kapena yabwino kuposa ya mango a Kalimantan. Ndikovuta kuthyola mango a Kalimantan chifukwa amakhala patali, mitengo yake imatalika kwambiri – mango amene amagwa pansi samakhala abwino.
Mangowa akhonza kudyedwa ongochoka mumtengo (ngati chipatso) kapena kuwapanga ngati jam wa Kasturi. Koma izi sizimagulitsidwa kawirikawiri pamsika, pakuti alimi amadya okha. Zinthu zina zimene zimapangidwa kuchokera m’mango ndi puree, jam, juice kapena dodol (zakudya zakuderako). Komabe zinthu zimenezi ndizovuta kuzipeza pakuti zipatso (mango) zenizenizo ndizimene zimafunidwa kwambiri ndikutinso ndi amodzi mwa zipatso zokondedwa kwambiri ndi anthu aku Banjar. Mangowanso ndiwodula koma kwa anthu aku Banjar samaona vuto chifukwa chakukoma kwa mangowa!
««« Nkhani ya m’mbuyo: Mango aku Indonesia Nkhani yotsatira: Kudzala nthanga za mango »»»
Lolemba 21. November 2011 19:55 | purintani | Zomera za chilendo
Mbiri ya KPR
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.
Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi