Kalimidwe ka Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia)
The Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia) ndizomera mmadzi zimene masamba ake amaoneka ngati clover. Mukuganiza kuti pakati pa zomera zammadzi ndi clover palibe ubale? Mbali ina – zonse mwa zinthuzi zikukamba za chikhalidwe cha zomera zosapezekapezeka zokongola kwambiri mu ulimi.
Four Leaf Clover ili ndi mizu yaitali, yomuganiziritsa munthu za zingwe za nsapato.masamba amene amayandama pamadzi, amamera kuchokera pa mizu. Masamba amenewa anagawikana panayi, kuoneka ngati four-leaf clover. Muvuula mizu mmadzi nthawi ya autumn, tinthu ting’ono-ting’ono timaoneka (tooneka ngati tinyemba). Four Leaf Clover amamera mmadzi ongoyima, madzi okhala ndi manyowa ambiri, m’maiko onse, kupatula South America.
Ku Amerika, chomera ichi chimatengedwa ngati chosafunika. Ku Slovakia, chomera ichi chimamera malo asanu ndi awiri m’mphepete mwa mtsinje wa Latorica. Kale, zinkapezeka m’dera la River Bodrog, Laborec ndi Uh.
M’madera otentha muli mitundu ina yofanana, nthawi zina imadzalidwa m‘ma aquarium.
Kukolora Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia), sikulira zambiri ndipo zomera zimenezi zimakula bwino kwambiri ndi mphika uliwonse malingana pansi pake pakuthilidwa madzi ndi dothi pang’ono. Mukhonza kulima mbewuyi popanda vuto mumphika wa 20×20×20 cm, koma kwenikweni mphika ukhale 60–80 liters kapena kuposera. Mukhonzanso kusunga mbewuyi panja chaka chonse (poti imalora ngakhale madzi owundana chifukwa chakuzizira kwambiri). Popeza simbewu yofuna zambiri, ndipo yosavuta kukula, aliyense akhonza kuyilima.
Four Leaf Clover amakula bwino koposa padziwe la m’munda. Tangoyikani dothi pang’ono la mmunda mwanu pansi pa dziwe – ndipo ikani muzu m’dothilo. Mukatha kutero, chisamaliro chimene chimafunika ndichochepa, poti Four Leaf Clover amadziyang’anira yekha. Four Leaf Clover sadzavutika kuzolowera malire a madzi ndipo kuchuluka kwa madzi kulibe vuto. Mukhonza kuthandiza mbewuyi kufalikira pogawagawa mizu yake. Mizu yochepa (kuzungulira 10cm) ndiyokwanira kupanga mphasa ya Four Leaf Clover m’madzi.
««« Nkhani ya m’mbuyo: Kudzala nthanga za mango Nkhani yotsatira: Pongamia pinnata »»»
Lachitatu 23. November 2011 19:58 | purintani | Malangizo a kalimidwe ka mbewu
Mbiri ya KPR
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.
Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi