Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Kulima bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus)

Bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus) ndi wotchuka kuposa bowa wamba (champignon mushroom)! tsopano. Kutengera ndi bowa wamba, bowa wa mzikuni uli ndi ubwino umodzi waukulu – sungasokonezedwe ndi chinthu chokupha (Amanita phalloides).

Bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus) uli ndi mavitamini ambiri, madzimadzi a thupi ndi chakudya cholimbitsa thupi zomwe zimateteza thupi ku zinthu zakupha kapena za poizoni. Umathandizanso kuchepetsa zonenepetsa zopezeka m’magazi ndipo ndiwofunika kugwiritsa ntchito m’madyedwe poti uli ndi zonenepetsa zochepa. Umakhulupiliridwa kuti uli ndi zinthu zoteteza ku matenda a khansa.

Malangizo pa kalimidwe ka bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus)

Bowa wa mzikuni ukhonza kulimidwa m’njira ziwiri – kuulima pa udzu odula (mapesi) m‘matumba a pulasitiki, kapena pa zipika za nkhuni.

Kulima pa udzu odula/mapesi m‘matumba a pulasitiki

Choyambilira ndi kukonza mapesi kapena udzu. Udzuwo uyenera kuwiritsidwa kuti tizirombo tife. Kuwiritsa kuli m’njira ziwiri;

  1. Ikani udzu kapena mapesi mu mphika waukulu ndikuthira madzi mpaka aphimbe udzuwo. Phikani ndipo temperature ikhale 100°C. Tsopano usiyeni udzuwo uzizire kufikira temperature yokwana 20–25°C.
  2. Njira yachiwiri (ndiponso yosavuta) ndiyotere; ikani mapesi kapena udzu mu mphika waukulu ndipo thirani madzi owira pamwamba pake. Maudzu / mapesi tsopano akhonza kugwiritsidwa ntchito akazizira temperature yokwana yokwana 20–25°C.

Tsopano yalani mapesi kapena udzu ndi bowa m‘matumba akulu a pulasitiki – leya ya mapesi/udzu, leya ya mycelium, leya ya mapesi/udzu, leya ya mycelium – choncho kumangotero. Thumba limodzi la mycelium ndilokwanira 15–20 kg udzu/mapesi onyowa (izi zimakwana pafupifupi thumba la 50×100cm). Thumba likadzadza, limangeni ndipo libooleni malo okwana khumi a pafupifupi 3–5 cm bowo lili lonse.

Ngati mungalime bowa wa mzikuni pa chinyezi, mukhonza kuboola malo ochepa (pakapita kanthawi mukhonza kupanga mabowo ambiri ngati kuli koyenera) kupewa kuti udzu/mapesi angaume. Mukadzala, ikani matumba panthunzi poopetsa dzuwa.

Temperature yabwino kulima bowa wa mzikuni ndiyapakati pa 15 ndi 20°C. Temperature ikakwera, bowa wa mzikuni umakula msanga. (ngakhale mapesi/udzu zimauma mwansanga ndi temperature yokwera).

Pachifukwa ichi ndi bwino kuti bowawu uzigwirizana ndi temperature. Ngati bowa wa mzikuniwapanga ma fangi ambiri kuposa m’mene umafunikira pa nthawiyi, uyikeni malo ozizira. Ngati mukufuna fangi wambiri, uikeni potentha! Pakatha miyezi itatu mpaka inayi bowa wa mzikuni umapanga bowa, pomwe chakudya cha mbewu m’thumba chatha ndipo mukufuna kupanganso wina watsopano (izi mukhonza kuchita pogwiritsa ntchito mapesi kapena udzu omwe munagwiritsa ntchito kale). Thumba limodzi lidzakupatsani pafupifupi 2–4 kg ya bowa wa mzikuni.

Kulima pa zipika za nkhuni

Mchilengedwe, bowa wa mzikuni umamela pa mitengo ya masamba. Pachifukwa ichi, mukhonzanso kuulima pa chikuni cha 30–80 cm. Mukhonza kugwiritsa ntchito zikuni kapena matabwa a mitengo ya masamba yosiyanasiyana yambiri. Nkhuni yake isakhale yopyola miyezi isanu ndi umodzi. Pali njira zambiri zodzalira bowa wa mzikuni pa chikuni / thabwa. Ndibwino kuti bowawu uzikhudzana ndi thabwa kuti mafangi amene ali mchikuni akule. Ikani mitengo ya mycelium m’dothi la 1/3 m’munda/m’dimba mwanu pamthunzi. Ngati zauma, nyowetsani ndi madzi. M‘mitengoyi mudzamela bowa m’zaka ziwiri mpaka zisanu (kutengera ndi chakudya chimene mtengowo uli nacho).

Kugulitsa bowa wa mycelium wa mzikuni

««« Nkhani ya m’mbuyo: Pongamia pinnata Nkhani yotsatira: Kudzala mababu a maluwa ndi mmera »»»

Lachisanu 25. November 2011 15:00 | purintani | Bowa

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi