Pinus kesiya - Khasi Pine, Paini wa Khasi
Khasi Pine, Paini wa Khasi (Pinus kesiya) ndi mtundu wa mitengo okula mwachangu ochokera ku Asia, umene sumapezeka ukulimidwa kawirikawiri kunja kwa dziko lake. Mitengo yake imakhala pakatikati pa mamita 30–35 kutalika kwake ndipo thunthu lamtengo chikhonza kukwana mitala imodzi mu dayamita (diameter). Nthambi iliyonse ili ndi tinthambi ting’onoting’ono titatu – iliyonse yotalika masentimitala 15 mpaka 20. Zipatso za mitengo imeneyi (zibalobalo za mtengo wa paini) zimakhala zazitali ma sentimitala 5 mpaka 9 ndipo njere zake zimakhala zazitali masentimitala 1.5 mpaka 2.5.
Kochokera kwa mitengo ya Kesha Pine (Paini wa Khasi, Pinus kesiya) ndiku dera la Himalaya: kuchokera ku mpoto chakum’mawa kwa India (masiku ano chifukwa cha chakudula nkhuni kokha ku phiri la Khasi ndi la Naga mu Meghalay ndi Manipur), China (dera la Yunnan), Burma (Myanmar), kumpoto kwa Thailand, Laos, Vietnam (Lai Chau, Lang Son, Cao Bang, Quang Ninh) ndi ku Philippines (Luzon). Mapaini ochokera ku Philippines amakonda kudziwika ngati mtundu wapadera wotchedwa Pinus insularis. Ku China wina anapeza mtundu wofanana ndi umenewu wotchedwa Yunnan Pine (Pinus yunnanensis).
Mtundu umenewu umapezeka malo otsetsereka pamodzi ndi mitengo ina yosiyanasiyana yomera mu dothi lachabe lofiira ndi lachikasu lokhala ndi acidi (lokhala ndi pH wa 4.5) ndipo yaitali mamitala 800–2000 koma kwenikweni mamitala 1200–1400. Derali lili ndi nyengo yake yosinthasintha nthawi yonyowa ndi youma pa chaka. Mvula yake imakhala yambiri ndipo nyengo yake kuderali ndiyosinthasintha ndiponso pali kusinthika kwa kanyowedwe ndi kawumidwe kake muchaka chili chonse ndi mvula yambiri ndi chifungafunga choposa 70%.
Mbewu iyi siyimalora mphepo yozizira kwambiri, koma imakonda mphepo yobwera mochedwa mu nthawi ya dzinja. Nthawi ya dzinja, mbewu imeneyi imafunikirabe dera lopanda mphepo yozizira kwambiri.
Mayina ena a mbewuyi: Pinus khasya, Pinus khasyanus
««« Nkhani ya m’mbuyo: Palmu Parajubaea torallyi (Palma Chico, coconut wam’phiri la Bolivian) Nkhani yotsatira: Mitengo ya palmu Rhapidophyllum hystrix yoyanjana ndi mphepo yozizira kwambiri (Ma Needle Palm) »»»
Lachiwiri 19. May 2009 18:22 | purintani | Zomera za chilendo
Mbiri ya KPR
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.
Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi