Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Kudzala kapinga watsopano

Nthawi yabwino yodzala kapinga kapena udzu owonjezera pa kapinga yemwe alipo kale ku Ulaya ndi kuchokera mwezi wa Meyi mpaka Juni. Julaye akhonza kukhala nthawi yabwino kudzala ngati kuli mvula.

Kumbani masentimitala a pakati pa 20 ndi 25 pamalo pomwe mukufuna kudzala kapinga. Mukhonza kusalaza dothi ndi chigayo chosalazila pa malo.

Tsono muli ndi kuthekera kuwiri

  1. Kudzala mbewu ya udzu

Choyambilira muyenera kuyeza malo omwe mukufuna kudzalapo kenaka werengani mbewu zomwe zikufunikira. Dziwani kuti pafunika mbewu yokwana magalamu makumi awiri ndi mphambu zisanu pa sikweya mitala imodzi. Pafunikanso magalamu makumi awiri ndi mphambu zisanu zoonjezera pa masikweya mitala khumi. Pogula mbewu onetsetsani kuti ndi yaiwisi poti udzu sumachedwa kutsika mphamvu ya kameredwe. (Mphamvu ya kameredwe ka mbewu yomwe yakhala zaka ziwiri imatsika ndi maperesenti makumi asanu). Chonde mvetserani za momwe mbewu imasungidwira mu shopu. (Mutha kupewa zinthu zokhumudwitsa posagula mbewu yonyowa kapena yomera kale. Mtengo wa mbewu ya udzu ndi 3 € pa kilogaramu imodzi (malingana ndi mtundu wake).

Sankhani mbewu zanu malingana ndi ntchito yake ya kukhumba kwanu (muzingoyendapo, kuthamangapo, kupangirapo masewero olimbitsa thupi kapena kugwiritsapo ntchito nyama). Ogulitsa odalirika adzakhala ndi mapepala a malangizo okuthandizani pakasankhidwe kanu ka mbewu pakati pa mbewu zazikulu. Masitolo odalirika amapereka mapepala a malangizo a kadzalidwe ka mbewu imene mwagula kwa makasitomala awo akafunsa. Osagula mbewu opanda cholinga.

Mukagula mbewuyi, iyikeni malo owuma ndi ozizira. Timanenetsa kuti musasunge mbewu kuposera chaka chimodzi pakuti imaluza mphamvu ya kameredwe. Fesani mbewu m’mwezi wa Meyi kapena Juni. Musanafese gwiritsani ntchito chipangizo chosalazira nthaka (rake) ndikupanga mphako m’dothi zakuya 1cm. Mukatha kudzala, salazani malowo (ndi chipangizo chosalazira nthaka (rake) mwachitsanzo ndikuthirirapo bwino. Pakatha masiku khumi ndi anayi, mbewu idzayamba kuphuka. Tchetchani udzu koyamba ngati wakula ndi masentimitala khumi. Dzalani wina ngati sunamere bwino. Ngati mukufuna udzu wabwino, tchetchani kamodzi kapena kawiri pa sabata ili yonse mpaka mwezi wa Sepitembala.

  1. Kugwiritsa tchito matailosi a kapinga pa bwalo lanu

Iyi ndi njira yachangu koma yodula. Ndiyabwino kwambiri chifukwa makampani ambiri amene amagulitsa matailosiwa, amatchaja mtengo pamodzi ndi kayalidwe kake. Mtengo wa matayilosiwa, kuphatikizapo ntchito, ndi kuzungulira 5 € pa sikweya mitala imodzi (malingana ndi mtundu wake).

2. Kakonzedwe ka bwalo la kapinga wa kale

Salazani malo onse pochotsa zinyalala kuyambira masamba ndi udzu onse owuma nyengo zonse za dzinja (malingana ndi mmene nyengo ilili ku Ulaya mumiyezi ya Marichi and Meyi). Ndipo dzalani mbewu ina yowonjezera ngati kuli kofunikira. Bwalo lanu likhonza kudzadza ndi madzi owundana chifukwa chakuzizira nthawi yozizira ndipo ndibwino kulisalaza nthawi ya dzinja.

Kukonza bwalo lanu kumapititsidwa patsogolo ndi mpweya wabwino wa munthaka. Ndi ichi, mukhonza kupanga chida chosavuta nokha. Tengani thabwa limodzi la 2–3 cm, likhomeni msomali wautali 10 cm mpaka utulukire mbali ina ya thabwalo. Onetsetsani kuti misomali yatalikirana 2–3 cm. Ikani chogwilira cha thabwa ku mbewu (kutalika kwake ngati msinkhu wanu kuti muchigwire bwino).

Tsopano tengani thabwa ndikuliyika pa bwalo (mukatha kutchetchapo) ndikuima mosagwedera pa thabwalo. Tsopano lichotseni ndikubwerenza njira yomweyi mpaka bwalo lonse likwane. Mukhonzanso kugwiritsa ntchito rake. Ngati mukufuna kuthilira kapinga wanu, mukhonza kuchita izi mutatha kuthilira. Madzi tsopano azifika pansi/pamizu mosavuta.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Kodi ndikugwetsa bwanji nankafumbwe wa nyemba? Nkhani yotsatira: Kodi mungatchetche bwanji bwalo lanu moyenera? »»»

Lolemba 14. November 2011 19:21 | purintani | Udzu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi