Tiyi waku China – Limani tiyi wanuwanu!

chithunzi

Maluwa a tiyi

Nyengo yozizira isanafike kumapeto, mlimi aliyense amaganizira za chomwe adzalime munyengo ikudzayo. Kodi mumaona kuti kulima tomato, paprika ndi minkhaka ndikosavuta? Kodi mukufuna china? China chachilendo? Mukuganiza bwanji pa zolima tiyi wanuwanu chaka chino?!

chithunzi

Kulima tiyi

Mbewu ya tiyi (Camellia) ili ndi mitundu makumi asanu (50) ya mitengo kapena mitengo ing’onoing’ono imene mwayonseyo tiyi waku China ndiamene ali otchuka kwambiri (Camellia sinensis). Mitengoyi inachokera kummwera ndi kummwera chakuvuma kwa China ndimaiko oyandikana nalo – India, Burma, Vietnam ndi Laos, kumene mbewuzi zikulimidwa kwa zaka zambiri. Ngakhale tiyiyu akulimidwa kumadera onse otentha, omwe amatulutsabe tiyi wambiri ndi aku China, Sri Lanka ndi Japan.

chithunzi

Njere za tiyi

Kulima tiyi wanuwanu ndikosavuta. Gawo lofunika kwambiri ndikugula mbewu yaiwisi, chifukwa mbewu ya tiyi imatha mphamvu msanga. Njere zake ndizozungulira. Musanadzale muyenera kuinyika mmadzi kwa masiku awiri kapena atatu. Mukatha izi, idzaleni m’dothi logwirizana ndi mbewuyi. Ndi temperature yokwana 20–25 ºC, njere zimamera m’milungu iwiri mpaka inayi. Ngati yadzalidwa pa malo adzuwa, mbewuyi imakula msanga ndipo ikhonza kubudulidwa ili ndi miyezi isanu ndi umodzi yokha.

M’madera otentha tiyi amatha kulimidwa m‘munda koma atha kusungidwa mnyumba kapena munkhokwe kumadera kumene madzi amaundana kamba kozizira. Chilimwe chotentha ndi madzi ambiri ndiye zinthu zofunikira kwambiri pa mbewu ya tiyi – izi ndi zimene zimachititsa kuyenda bwino kwa ulimi wa tiyi kumaiko kumene tiyi anachokera.

Ngati simukhala m’madera othentha, ngakhale kuti tiyi amene mumalima mmunda mwanu kapena mudimba lanu sakhala tiyi wabwino kwenikweni koma atalimidwa kumadera otentha, mudzasangalala pamene tiyiyu mwamusamalira ndikukhala ndi maluwa oyera akuluakulu okongola.

Ngati mumakhala m’madera amene madzi amaundana chifukwa chakuzizira, nthawi ya dzinja, muzidzala mbewu ya tiyi moyang’anana ndi masill a mawindo. Chifukwa chakuti tiyi amakhala wobiliwira nthawi zonse ndipo akhonza kukhala kuti sakupeza dzuwa lokwanira mnyengo yozizira, akhonza kufota ndi kuthothoka masamba. Ngakhale zili chomwechi, ndikubwera kwa nyengo yadzinja akhonza kubweleramo ndipo mukhonza kutolanso tiyi wanuwanu!

Printed from neznama adresa