Tsopano mitundu yosangalatsa ya zipatso za kumadera otentha ikutumizidwa ku Ulaya. Ndakwanitsa kugula chipatso cha mpoza ndikuchilawa. Sichipezeka m’mashopu a zipatso koma ndithokoze makondedwe anga, nachonso chipeza malo ake kumeneko!
Mipoza ndi maina otchulidwa kwambiri pa zipatso za Annona cherimola zomera m’zigwa za Andes kuchokera ku Colombia mpaka ku Peru pamtunda wa 700–2400 m. Umapiliranso matemperature wotsika kotero ukhonza kudzalidwa malo ambiri m’madera ena othentherapo padziko lonse – ngakhalenso ku Israel ndi kum‘mwera kwa Spain. Pamitundu imeneyi tikudziwa pafupifupi mitundu 120.
Mpoza uli ndi khungwa lokuda mobiliwira ndipo khungu lake ndilokhotakhota (losasalala) ngati kuti wina wake wasiyapo zidindo za zala zake. Zipatso zaziwisi zikhonza kusungidwa malo a temperature ya chipinda. Mnofu wa chipatso ndiwofewa, uli ndi mtundu wa kirimu ndipo umakoma ngati nthochi ndi/kapena nanazi. Mkati mwa mpoza muli njere zofiira 10–20 zazikulu ngati nyemba. Mpoza umadyedwa ngati chipatso ukapsya.
Mukhonza kudzala njere zake mnyumba mwanu kapena mudimba. Kumera kwake kumasiyana, koma nthawi zambiri kumatenga sabata imodzi kapena masabata atatu. Temperature yabwino kwambiri ndi kuzungulira 27 °C. Mbewu zazing’ono zili ndi mtundu wokongola, koma umasinthiratu kukhala wobiliwira kwambiri ndi masamba aubweya ozungulira ngati dzira atali 10–15 cm okhala ndi masamba ataliatali pambuyo pake.
Mnyengo ya dzinja mtengo wa mpoza umayoyoka masamba ndipo ukaonongeka umamveka fungo loipa. Nthambi zatsopano zimamera pamene masamba ayoyoka. Mitundu yonse ya mipoza imafuna kuwala kochuluka komanso njira yabwino yozembera mphepo (kuzizira) – iyi ndi mfundo yokambirana pakati pa olima! Ine ndimaika mipoza malo a temperature ya 10–15 ºC poopetsa kuzizira. Munyengo ya dzinja munthu akuyenera kuona kalimidwe ka zitsanzo za mbewu zosiyana pa temperature ya chipinda (room temperature), kuti aone imene ingayoyoke msanga.
Mpoza umayoyoka katatu mpaka kasanu pa chaka. Usanayambe kuyoyoka, mpoza umaoneka ofota ndipo umaluza pafupifupi masamba ake onse. Maluwa ake ndi achikasu cha bulawuni ndipo amayoyoka pomwe masamba agwa kapena kusasuka ndi kubwera kwa masamba atsopano
Musasokonozedwe ndi pamwamba pa mtengo pamene pamaoneka pofota nthawi zonse. Nyengo yochepa youma siyingaononge mbewu, koma zimafunanso madzi nyengo ya dzinja. Ngati muli ndi mwayi, mukhonzanso kugula imodzi mwa mitundu iyi:
Annona squamosa – mipoza yosenda ngati momwe timasendera nanazi. Imatchedwanso ma apozi a sugar ndipo zipatso zake zimakhala zobiliwira mwa chikasu.
Annona muricata – mipoza iyi imakhala yayikulu (1,5–5 kg) – khungu lake lili ndi tobaya topindika tatitali 0,5 cm. Ndiobiliwira. Masamba a mipoza imeneyi amapangira tiyi wa Corosol.
Printed from neznama adresa