Kodi ndikugwetsa bwanji nankafumbwe wa nyemba?

Sindikuyembekezera kuti simukuyenera kuuzidwa za nankafumbwe wa nyemba. Uyu ndi nankafumbwe wamkulu 3–4mm, amene amapezeka pa njere mukhitchini mwachitsanzo.

Anankafumbwe owonongawa amapangidwa kuchokera mmitundu ya makoko a njere kapena nthanga za zomera zosiyanasiyana. Tingoti, makoko aliwonse ali ndi zina mwa zirombozi – chitedze – nankafumbwe wa chitedze, sawawa – nankafumbwe wa sawawa, mseula – nankafumbwe wa mseula, ndi ena ambiri…

Pa njere zoonongeka pakhonza kukhala pokhukhuluzika malo amene mphutsi zinakumba mabowo. Pamene nankafumbwe wamkulu waswa, panjere pamayamba kuoneka mabowo. Nankafumbwe kawirikawiri amabweretsa mavuto ambiri nyengo yokolora mosaganizira kuti mbewu inali yowonongeka kale pamene inali m’munda.

Nkhondo ya nankafumbwe ubwino wake ndiyosavuta ndi yogonjetseka (100% mwayi wogonjetsera!)

chithunzi

nankafumbwe pa njere za Erythrina lysistemon

Mukangotha kuchotsa makoko a njere zokhwima, sendani ndikuziumitsa, ndipo onetsetsani kuti palibe njere zowonongeka pakati pawo. Tayani zonse zowonongeka (njira yabwino ndikuziwotcha). Mukatha ikani njere zanu muthumba la pulasitiki kapena lakotoni ndipo ziyikeni mu firiji malo owumitsa kwa maola makumi anayi ndi mphambu zisanu ndi zitatu (48 hours). Ndi njira iyi mukhonza kupha anankafumbwe amene amafuna kuyamba.

Muchotsa njere zanu mufirigi malo owumitsa, mukhonza kuziyanika kwa masiku awiri kapena atatu. Mukhonza kusiya njere zanu muthumba la pulasitiki mpaka nthawi imene mukufuna kugwiritsa ntchito. Njere zimene zimasungidwa m’njira iyi zikhonza kuwonongeka pokhapokha kuchokera ku njere zogulidwa ku shopu.

Pachifukwachi, ndibwino kusunga njere zanu m’botolo la galasi lotsekera. Njere ziume bwinobwino apo ayi, zidzaola. Ndi njira imeneyi mukhonza kuonetsetsa kuti njere zanu zisawonongeke ndi nankafumbwe.

Nankafumbwe akhonzanso kugonjetsedwa posankha mbewu yabwino – pali mitundu yambiri imene nankafumbwe samakonda.

Printed from neznama adresa